WA GANYU 2

WA GANYU 2 Always update

25/08/2023



M'modzi mwa oimba odziwika bwino m'dziko muno Lawrence Khwisa, yemwe amadziwika Ndi dzina lakuti "Lulu" wati anthu asamathamangile kudzikhweza akakhala ndi mavuto am'malingaliro.

Lulu wanena izi pomwe madzulo ano akuyembekezeka kutulutsa nyimbo yotchedwa "Okongola" yomwe waimba limodzi ndi Gwamba.

Iye wati nyimboyi ikulimbikitsa anthu kuthokoza Mulungu nthawi zonse.

25/08/2023
25/08/2023

MPONDA NDI MUNTHALI AKUYAMBA NTCHITO LERO

Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets wakale, Peter Mponda, ndi goloboyi wa Flames, Brighton Munthali, akuyamba ntchito yawo lero pomwe timu ya Black Leopards ikukumana ndi Pretoria Callies mu masewero oyamba a ligi ya Motsepe Foundation Championship ku South Africa.

Mponda anapita kutimuyi ngati wachiwiri kwa mphunzitsi miyezi iwiri yapitayo ndipo anasankha goloboyi wake wakale ku Sure Stream Academy komanso Wizards FC, Munthali, kuti akagwire nayenso ntchito mdzikoli.

Iwo anakapezako osewera wakale wa Wizards, Raffick Namwera, yemwe agwire nayenso ntchito mu ligi ya chaka chino. Timuyi inatuluka chaka chatha koma inagulanso malo ndipo imenyera nkhondo yoti ilowe mu ligi ya DSTV Premiership. Masewero omwe aliko lero ndi awa:

•La Masia 15:00 Upington City
•Pretoria Callies 15:00 Black Leopards
•Maritzburg United 19:30 Milford FC

Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr

Address

Lilongwe
Lilongwe
WAGANYU2

Telephone

+265990424480

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when WA GANYU 2 posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share